|
Makandulo 15,303 ochokera kumayiko 131 akuwala.
Mmiyambo yambiri kuyatsa kandulo ndi chinthu chodalitsika. Kuyatsa kandulo kumakhala ndi uthenga wamphamvu kuposela uthenga woperekedwa ndi mawu a pakamwa. Kuyatsa kandulo kumasonyeza kuyamika kwakukulu. Kuyambira kalekale anthu akhala akuyatsa makandulo mmalo odalitsika. Nanga njira yamauthenga odzera mumakina a komputa, imene muchizungu amati cyberspace singakhalenso yodalitsika?
Mungakhale wokondwa kuyamba ndi kutsiliza tsiku lanu ndi mwambo woyatsa kandulo pa web site ino. Mwinanso mungafune kuyatsa kandulo kwa amzanu pokumbukira tsiku lakubadwa kwawo. Ngati mukufuna kutero tsatirani njira iyi: Mukhale chete pakanthawi ndipo muganize ndi mtima wanu wonse zoyatsa kandulo potsata malangizo amene tikupatseni mwandondomeko kuyambira pano.
|